Ndipo mfumu Davide anatumiza kwa Zadoki ndi Abiyatara ansembewo, nati, Mulankhule nao akulu a Yuda, kuti, Mukhale bwanji am'mbuyo kubwera nayo mfumu kunyumba yake? Pakuti mau a Aisraele onse anafika kwa mfumu akuti abwere nayo kunyumba yake.
2 Samueli 19:41 - Buku Lopatulika Ndipo onani, Aisraele onse anafika kwa mfumu, nanena ndi mfumu, Abale athu anthu a Yuda anakuchotsani bwanji mwakuba, naolotsa mfumu ndi banja lake pa Yordani, ndi anthu onse a Davide pamodzi naye? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo onani, Aisraele onse anafika kwa mfumu, nanena ndi mfumu, Abale athu anthu a Yuda anakuchotsani bwanji mwakuba, naolotsa mfumu ndi banja lake pa Yordani, ndi anthu onse a Davide pamodzi naye? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka Aisraele onse adafika kwa mfumu, nadzafunsa kuti, “Chifukwa chiyani abale athu Ayuda achita ngati kukubani, nabwera ndi inu amfumu pamodzi ndi banja lanu ndi anthu anu onse, kuwoloka Yordani?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Aisraeli onse amabwera kwa mfumu nʼkumati kwa iye, “Nʼchifukwa chiyani abale athu, anthu a ku Ayuda, anakubani mfumu, nawoloka nanu Yorodani inu ndi banja lanu, pamodzi ndi anthu ake onse?” |
Ndipo mfumu Davide anatumiza kwa Zadoki ndi Abiyatara ansembewo, nati, Mulankhule nao akulu a Yuda, kuti, Mukhale bwanji am'mbuyo kubwera nayo mfumu kunyumba yake? Pakuti mau a Aisraele onse anafika kwa mfumu akuti abwere nayo kunyumba yake.
Inu ndinu abale anga, muli fupa langa ndi mnofu wanga; chifukwa ninji tsono muli am'mbuyo koposa onse kubwera nayo mfumu?
Ndipo tsiku lija anthu analowa m'mzinda kachetechete, monga azemba anthu akuchita manyazi pakuthawa nkhondo.
Pamenepo amuna a Efuremu analalikidwa, napita kumpoto; nati kwa Yefita, Wapitiriranji kuthira nkhondo ana a Amoni, osatiitana ife timuke nawe? Tidzakutenthera nyumba yako ndi moto pamutu pako.
Ndipo amuna a Efuremu anati kwa iye, Ichi watichitira nchiyani, osatiitana popita iwe kulimbana ndi Amidiyani? Natsutsana naye kolimba.