Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 19:4 - Buku Lopatulika

Ndipo mfumu inafunda nkhope yake, nilira ndi mau okweza, Mwana wanga Abisalomu, Abisalomu, mwana wanga, mwana.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo mfumu inafunda nkhope yake, nilira ndi mau okweza, Mwana wanga Abisalomu, Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga,

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mfumu idaphimba kumaso, nimalira kuti, “Kalanga ine, mwana wanga Abisalomu, iwe Abisalomu mwana wanga, mwana wanga!”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mfumu inaphimba nkhope yake ndipo inalira mofuwula, “Iwe mwana wanga Abisalomu! Iwe Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!”

Onani mutuwo



2 Samueli 19:4
5 Mawu Ofanana  

Ndipo Yowabu mwana wa Zeruya anazindikira kuti mtima wa mfumu unalunjika kwa Abisalomu.


Ndipo Davide anakwera pa chikweza cha ku Azitona nakwera nalira misozi; ndipo anafunda mutu wake nayenda ndi mapazi osavala; ndi anthu onse amene anali naye anafunda munthu yense mutu wake ndipo anakwera, nalira misozi pokwerapo.


Ndipo mfumuyo inagwidwa chisoni, nikwera ku chipinda chosanja pa chipatacho, nilira misozi; niyenda, nitero, Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu; mwana wanga! Mwenzi nditakufera ine, Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!


Ndipo tsiku lija anthu analowa m'mzinda kachetechete, monga azemba anthu akuchita manyazi pakuthawa nkhondo.


Ndipo Yowabu anafika kunyumba ya mfumu, nati, Lero mwachititsa manyazi nkhope zao za anyamata anu onse, amene anapulumutsa moyo wanu lero, ndi miyoyo ya ana anu aamuna ndi aakazi, ndi miyoyo ya akazi anu, ndi miyoyo ya akazi anu aang'ono;