Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 19:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Mfumu inaphimba nkhope yake ndipo inalira mofuwula, “Iwe mwana wanga Abisalomu! Iwe Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 Ndipo mfumu inafunda nkhope yake, nilira ndi mau okweza, Mwana wanga Abisalomu, Abisalomu, mwana wanga, mwana.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo mfumu inafunda nkhope yake, nilira ndi mau okweza, Mwana wanga Abisalomu, Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Mfumu idaphimba kumaso, nimalira kuti, “Kalanga ine, mwana wanga Abisalomu, iwe Abisalomu mwana wanga, mwana wanga!”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 19:4
5 Mawu Ofanana  

Yowabu mwana wa Zeruya anadziwa kuti maganizo a mfumu ali pa Abisalomu.


Koma Davide anapitirira ndi kukakwera phiri la Olivi akupita nalira. Anafunda kumutu koma sanavale nsapato. Anthu onse amene anali naye anafundanso kumutu, ndipo nawonso amalira pamene amapita.


Mfumu inanthunthumira. Inapita ku chipinda cha mmwamba cha pa chipata kukalira. Pamene imapita, inkati: “Iwe mwana wanga Abisalomu! Mwana wanga! Mwana wanga Abisalomu! Zikanakhala bwino ndikanafa ndine mʼmalo mwako! Iwe Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!”


Ankhondo analowa mu mzinda mwakachetechete tsiku limenelo ngati momwe amalowera anthu mwamanyazi chifukwa athawa ku nkhondo.


Kenaka Yowabu analowa mʼnyumba ya mfumu nafika kwa mfumuyo ndipo anati, “Lero mwachititsa manyazi asilikali anu onse, amene apulumutsa moyo wanu ndiponso moyo wa ana anu aamuna ndi aakazi, kudzanso moyo wa akazi anu ndi wa azikazi anu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa