Ndipo mfumu inanena ndi Barizilai, Tiyeni muoloke nane, ndipo ndidzakusungani pamodzi ndi ine ku Yerusalemu.
2 Samueli 19:34 - Buku Lopatulika Koma Barizilai ananena ndi mfumu, Masiku a zaka za moyo wanga ndiwo angati, kuti ndiyenera kukwera ndi mfumu kunka ku Yerusalemu? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Barizilai ananena ndi mfumu, Masiku a zaka za moyo wanga ndiwo angati, kuti ndiyenera kukwera ndi mfumu kunka ku Yerusalemu? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Barizilai adafunsa mfumu kuti, “Kodi ine zanditsalira zaka zingati zokhalabe moyo, kuti ndingapite nanu amfumu ku Yerusalemu? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Barizilai anayankha mfumu kuti, “Kodi zakhala zaka zingati zoti ndikhale ndi moyo, kuti ndipite ku Yerusalemu ndi mfumu? |
Ndipo mfumu inanena ndi Barizilai, Tiyeni muoloke nane, ndipo ndidzakusungani pamodzi ndi ine ku Yerusalemu.
Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi? Ndikadayembekeza masiku onse a nkhondo yanga, mpaka kwafika kusandulika kwanga.
Koma ichi nditi, abale, yafupika nthawi, kuti tsopano iwo akukhala nao akazi akhalebe monga ngati alibe;
inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.