2 Samueli 19:35 - Buku Lopatulika35 Lero ndili nazo zaka makumi asanu ndi atatu; kodi ndikhoza kuzindikiranso kusiyanitsa zabwino ndi zoipa? Mnyamata wanu ndikhoza kodi kuzindikira chimene ndidya kapena kumwa? Kodi ndikhozanso kumva mau a amuna ndi akazi oimba? Chifukwa ninji tsono mnyamata wanu ndidzakhalanso wolemetsa mbuye wanga mfumu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201435 Lero ndili nazo zaka makumi asanu ndi atatu; kodi ndikhoza kuzindikiranso kusiyanitsa zabwino ndi zoipa? Mnyamata wanu ndikhoza kodi kuzindikira chimene ndidya kapena kumwa? Kodi ndikhozanso kumva mau a amuna ndi akazi oimba? Chifukwa ninji tsono mnyamata wanu ndidzakhalanso wolemetsa mbuye wanga mfumu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa35 Tsopano ine zaka zanga zakwana 80. Kodi ndingathe kusiyanitsa zinthu zokondwetsa ndi zosakondwetsa? Kodi ine mtumiki wanu ndingathe kuzindikira kukoma kwake kwa zakudya kapena zakumwa? Kodi ine ndingathebe kumamvera kuimba kwa amuna ndi kwa akazi? Chifukwa chiyani ine mtumiki wanu ndikakhale ngati katundu wolemera wosanjikiza pa inu, mbuyanga mfumu? Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero35 Ine tsopano ndili ndi zaka 80. Kodi ndingathe kusiyanitsa pakati pa chabwino ndi choyipa? Kodi mtumiki wanu angathe kuzindikira kukoma kwa zimene akudya ndi kumwa? Kodi ndingathe kumva kuyimba kwa amuna ndi akazi? Nʼchifukwa chiyani wantchito wanu akakhale ngati katundu kwa mbuye wanga mfumu? Onani mutuwo |