Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 19:30 - Buku Lopatulika

Ndipo Mefiboseti anati kwa mfumu, Lingakhale lonselo alitenge, popeza mbuye wanga mfumu wabwera mumtendere kunyumba yake.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Mefiboseti anati kwa mfumu, Lingakhale lonselo alitenge, popeza mbuye wanga mfumu wabwera mumtendere kunyumba yake.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Koma Mefiboseti adauza mfumu kuti, “Mloleni mnzangayu kuti atenge ndiye chuma chonsecho. Kwa ine kwakwana kuti inu mbuyanga mfumu mwafika kwanu kuno mwamtendere.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mefiboseti anati kwa mfumu, “Muloleni atenge zonse, pakuti tsopano mbuye wanga mwafika kwanu mu mtendere.”

Onani mutuwo



2 Samueli 19:30
7 Mawu Ofanana  

Ndipsinjika mtima chifukwa cha iwe, mbale wanga Yonatani; wandikomera kwambiri; chikondi chako, ndinadabwa nacho, chinaposa chikondi cha anthu aakazi.


Ndipo ngalawa yakuolotsera inaoloka kuti akatenge banja la mfumu ndi kuchita chomkomera. Ndipo Simei mwana wa Gera anagwa pansi pamaso pa mfumu pakuoloka iye pa Yordani.


Ndipo mfumu inanena naye, Ulikulankhulanso bwanji za zinthu zako? Ine ndikuti, Iwe ndi Ziba mugawe dzikolo.


Ndipo Barizilai, Mgiliyadi anatsika kuchokera ku Rogelimu; nayambuka pa Yordani ndi mfumu, kuti akamuolotse pa Yordani.


Pomwepo mfumu inaitana Ziba, mnyamata wa Saulo, ninena naye, Za Saulo zonse ndi za nyumba yake yonse ndampatsa mwana wa mbuye wako.


Komatu sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.


monga mwa kulingiriritsa ndi chiyembekezo changa, kuti palibe chinthu chidzandichititsa manyazi, komatu mwa kulimbika mtima konse, monga nthawi yonse, tsopanonso Khristu adzakuzidwa m'thupi langa, kapena mwa moyo, kapena mwa imfa.