Ndipo Yowabu mwana wa Zeruya anazindikira kuti mtima wa mfumu unalunjika kwa Abisalomu.
2 Samueli 19:2 - Buku Lopatulika Ndipo chipulumutso cha tsiku lija chinasandulika maliro kwa anthu onse; pakuti anthu anamva kuti, Mfumu ili ndi chisoni chifukwa cha mwana wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo chipulumutso cha tsiku lija chinasandulika maliro kwa anthu onse; pakuti anthu anamva kuti, Mfumu ili ndi chisoni chifukwa cha mwana wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho chikondwerero cha tsikulo chidasanduka maliro kwa anthu onse, pakuti anthu adamva kuti mfumu ili pa chisoni chachikulu chifukwa cha mwana wake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo kwa asilikali onse chipambano cha tsiku limenelo chinasandulika maliro, chifukwa tsiku limenelo anthu anamva kuti mfumu ili pa chisoni chachikulu chifukwa cha mwana wake. |
Ndipo Yowabu mwana wa Zeruya anazindikira kuti mtima wa mfumu unalunjika kwa Abisalomu.
Ndipo tsiku lija anthu analowa m'mzinda kachetechete, monga azemba anthu akuchita manyazi pakuthawa nkhondo.
M'kuunika kwa nkhope ya mfumu muli moyo; kukoma mtima kwake kunga mtambo wa mvula ya masika.
Mkwiyo wa mfumu ukunga kubangula kwa mkango; koma kukoma mtima kwake kunga mame pamsipu.