2 Samueli 18:6 - Buku Lopatulika Chomwecho anthuwo anatulukira kuthengo kukamenyana ndi Israele; nalimbana ku nkhalango ya ku Efuremu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chomwecho anthuwo anatulukira kuthengo kukamenyana ndi Israele; nalimbana ku nkhalango ya ku Efuremu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ankhondo adatuluka kunka ku thengo kukamenyana ndi Aisraele. Ndipo nkhondo idachitikira ku nkhalango ya Efuremu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ankhondo anayenda kupita kukachita nkhondo ndi Israeli, ndipo nkhondo inachitika mʼnkhalango ya Efereimu. |
Ndipo anthu a Israele anakanthidwa pamenepo pamaso pa anyamata a Davide, ndipo kunali kuwapha kwakukulu kumeneko tsiku lomwelo, anthu zikwi makumi awiri.
Ndipo Yoswa ananena nao, Ngati muli anthu aunyinji, kwerani kuli mitengoko, ndi kudziswera minda m'dziko la Aperizi ndi la Arefaimu; akakucheperani malo kuphiri la Efuremu.
koma kuphiriko kudzakhala kwanu pakuti pangakhale mpa mitengo, mudzisweretu minda, ndi matulukiro ake adzakhala anu; pakuti mudzaingitsa Akanani angakhale ali nao magaleta achitsulo, angakhale ali amphamvu.