Ndipo wina anauza Davide nati, Ahitofele ali pakati pa opangana chiwembu pamodzi ndi Abisalomu. Davide nati, Yehova, musandulize uphungu wa Ahitofele ukhale wopusa.
2 Samueli 17:7 - Buku Lopatulika Ndipo Husai ananena ndi Abisalomu, Uphungu anaupangira lero Ahitofele suli wabwino. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Husai ananena ndi Abisalomu, Uphungu anaupangira lero Ahitofele suli wabwino. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Husai adauza Abisalomu kuti, “Ulendo uno, malangizo amene wakupatsani Ahitofele si abwino konse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Husai anayankha Abisalomu kuti, “Malangizo amene Ahitofele wapereka si abwino pa nthawi ino. |
Ndipo wina anauza Davide nati, Ahitofele ali pakati pa opangana chiwembu pamodzi ndi Abisalomu. Davide nati, Yehova, musandulize uphungu wa Ahitofele ukhale wopusa.
koma ukabwerera kumzinda, ndi kunena ndi Abisalomu, Ine ndine mnyamata wanu, mfumu; monga kale ndinali mnyamata wa atate wanu, momwemo tsopano ndidzakhala mnyamata wanu; pomwepo udzanditsutsira uphungu wa Ahitofele.
Ndipo Ahitofele ananena ndi Abisalomu, Mulowe kwa akazi aang'ono a atate wanu amene iye anawasiya kuti asunge nyumbayo; ndipo Aisraele onse adzamva kuti atate wanu aipidwa nanu; pomwepo manja a onse akukhala nanu adzalimba.
Ndipo pakufika Husai kwa Abisalomu, Abisalomuyo ananena naye, Ahitofele analankhula mau akuti; tichite kodi monga mwa kunena kwake? Ngati iai, unene ndiwe.