Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 17:7 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Husai anayankha Abisalomu kuti, “Malangizo amene Ahitofele wapereka si abwino pa nthawi ino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

7 Ndipo Husai ananena ndi Abisalomu, Uphungu anaupangira lero Ahitofele suli wabwino.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo Husai ananena ndi Abisalomu, Uphungu anaupangira lero Ahitofele suli wabwino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Husai adauza Abisalomu kuti, “Ulendo uno, malangizo amene wakupatsani Ahitofele si abwino konse.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 17:7
5 Mawu Ofanana  

Tsono Davide anamva kuti, “Ahitofele ali pakati pa anthu owukira pamodzi ndi Abisalomu.” Choncho Davide anapemphera, “Inu Yehova, musandutse uphungu wa Ahitofele ukhale uchitsiru.”


Koma ngati ubwerera ku mzinda ndi kukanena kwa Abisalomu kuti, ‘Inu mfumu ine ndidzakhala wantchito wanu.’ Mʼmbuyomu ndinali wantchito wa abambo anu koma tsopano ndidzakhala wantchito wanu. Ukatero udzandithandiza kulepheretsa malangizo a Ahitofele.


Ahitofele anayankha kuti, “Mugone ndi azikazi a abambo anu amene awasiya kuti asamalire nyumba yaufumu. Aisraeli onse adzamva kuti mwachitira abambo anu chinthu chonyansa kotheratu ndipo anthu onse amene ali ndi iwe adzalimbikitsidwa.”


Husai atabwera kwa iye, Abisalomu anati, “Ahitofele wapereka malangizo ake. Kodi tichite zimene wanena? Ngati sichoncho, tiwuze maganizo ako.”


Yankhula mʼmalo mwa amene sangathe kudziyankhulira okha. Uwayankhulire anthu onse osiyidwa pa zonse zowayenera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa