Pomwepo Abisalomu anati, Kaitane tsopano Husai Mwariki yemwe, timvenso chimene anene iye.
2 Samueli 17:6 - Buku Lopatulika Ndipo pakufika Husai kwa Abisalomu, Abisalomuyo ananena naye, Ahitofele analankhula mau akuti; tichite kodi monga mwa kunena kwake? Ngati iai, unene ndiwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pakufika Husai kwa Abisalomu, Abisalomuyo ananena naye, Ahitofele analankhula mau akuti; tichite kodi monga mwa kunena kwake? Ngati iai, unene ndiwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Husai atabwera kwa Abisalomu, Abisalomuyo adamuuza kuti, “Zimene wanena Ahitofele nzimenezi, kodi tichitedi monga m'mene watilangiziramo? Ngati si choncho, iweyo utiwuze chochita.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Husai atabwera kwa iye, Abisalomu anati, “Ahitofele wapereka malangizo ake. Kodi tichite zimene wanena? Ngati sichoncho, tiwuze maganizo ako.” |
Pomwepo Abisalomu anati, Kaitane tsopano Husai Mwariki yemwe, timvenso chimene anene iye.