Ndipo Abisalomu anaika Amasa, kazembe wa khamulo, m'malo a Yowabu. Koma Amasayu ndiye mwana wa munthu dzina lake Yetere Mwismaele, amene analowa kwa Abigaile, mwana wamkazi wa Nahasi, mlongo wa Zeruya, amai a Yowabu.
2 Samueli 17:26 - Buku Lopatulika Ndipo Israele ndi Abisalomu anamanga zithando m'dziko la Giliyadi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Israele ndi Abisalomu anamanga zithando m'dziko la Giliyadi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Aisraele pamodzi ndi Abisalomu adamanga zithando zankhondo m'dziko la Giliyadi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aisraeli ndi Abisalomu anamanga zithando mʼdziko la Giliyadi. |
Ndipo Abisalomu anaika Amasa, kazembe wa khamulo, m'malo a Yowabu. Koma Amasayu ndiye mwana wa munthu dzina lake Yetere Mwismaele, amene analowa kwa Abigaile, mwana wamkazi wa Nahasi, mlongo wa Zeruya, amai a Yowabu.
Ndipo kunali pakufika Davide ku Mahanaimu, Sobi mwana wa Nahasi wa ku Raba wa ana a Amoni, ndi Makiri mwana wa Amiyele wa ku Lodebara, ndi Barizilai Mgiliyadi wa ku Rogelimu,
Chomwecho anthuwo anatulukira kuthengo kukamenyana ndi Israele; nalimbana ku nkhalango ya ku Efuremu.
Gawo la fuko la Manase ndi ili: pakuti anali woyamba wa Yosefe. Makiri mwana woyamba wa Manase, atate wa Giliyadi, popeza ndiye munthu wa nkhondo, anakhala nayo Giliyadi ndi Basani.