koma ukabwerera kumzinda, ndi kunena ndi Abisalomu, Ine ndine mnyamata wanu, mfumu; monga kale ndinali mnyamata wa atate wanu, momwemo tsopano ndidzakhala mnyamata wanu; pomwepo udzanditsutsira uphungu wa Ahitofele.
2 Samueli 17:20 - Buku Lopatulika Ndipo anyamata a Abisalomu anafika kunyumba kwa mkaziyo; nati, Ali kuti Ahimaazi ndi Yonatani? Ndipo mkaziyo ananena nao, Anaoloka kamtsinje kamadzi. Ndipo atawafunafuna, osawapeza, anabwerera kunka ku Yerusalemu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anyamata a Abisalomu anafika kunyumba kwa mkaziyo; nati, Ali kuti Ahimaazi ndi Yonatani? Ndipo mkaziyo ananena nao, Anaoloka kamtsinje kamadzi. Ndipo atawafunafuna, osawapeza, anabwerera kunka ku Yerusalemu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ankhondo a Abisalomu atabwera kwa mkaziyo kunyumba kuja, adamufunsa kuti, “Kodi mwaonako Ahimaazi ndi Yonatani pano?” Mkazi uja adaŵayankha kuti, “Amenewo aoloka mtsinjewu.” Koma ataŵafunafuna, osaŵapeza, ankhondowo adabwerera ku Yerusalemu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu a Abisalomu atafika kwa mkaziyo pa nyumbapo anafunsa kuti, “Kodi Ahimaazi ndi Yonatani ali kuti?” Mkaziyo anawayankha kuti, “Awoloka mtsinje.” Anthuwo anafunafuna koma sanapeze munthu, kotero anabwerera ku Yerusalemu. |
koma ukabwerera kumzinda, ndi kunena ndi Abisalomu, Ine ndine mnyamata wanu, mfumu; monga kale ndinali mnyamata wa atate wanu, momwemo tsopano ndidzakhala mnyamata wanu; pomwepo udzanditsutsira uphungu wa Ahitofele.
Ndipo anamwino ananena ndi Farao, Popeza akazi a Ahebri safanana ndi akazi a Aejipito; pakuti ali ndi mphamvu, naona ana asanafike anamwino.
Ndipo Sisera ananena naye, Taima pakhomo pa hema, ndipo kudzali, akadza munthu, akakufunsa akati, Pali munthu pano kodi? Uziti, Palibe.
Nati Davide kwa Ahimeleki wansembeyo, Mfumu inandilamulira ntchito, ninena nane, Asadziwe munthu aliyense kanthu za ntchito imene ndakutumira ndi kukulamulira; ndipo ndawapanga anyamatawo ku malo akuti.