Ndipo pakufika mfumu Davide ku Bahurimu, onani, panatuluka pamenepo munthu wa banja la nyumba ya Saulo, dzina lake ndiye Simei, mwana wa Gera; iyeyu anatulukako, nayenda natukwana.
2 Samueli 17:18 - Buku Lopatulika Koma mnyamata wina anawaona nauza Abisalomu; ndipo ajawo anachoka msanga onse awiri, nafika kunyumba ya munthu ku Bahurimu, amene anali nacho chitsime pabwalo pake; ndipo anatsikira m'menemo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma mnyamata wina anawaona nauza Abisalomu; ndipo ajawo anachoka msanga onse awiri, nafika kunyumba ya munthu ku Bahurimu, amene anali nacho chitsime pabwalo pake; ndipo anatsikira m'menemo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma tsiku lina mnyamata wina adaŵaona, nakauza Abisalomu. Choncho Yonatani ndi Ahimaazi adathaŵa mofulumira, nakafika ku Bahurimu ku nyumba ya munthu wina, amene anali ndi chitsime pakhomo pake. Aŵiriwo adatsikira m'chitsimemo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma mnyamata wina anawaona ndipo anakawuza Abisalomu. Kotero anthu awiriwo anachoka mofulumira ndipo anapita ku nyumba ya munthu wina ku Bahurimu. Iye anali ndi chitsime ku mpanda kwake ndipo iwo analowamo. |
Ndipo pakufika mfumu Davide ku Bahurimu, onani, panatuluka pamenepo munthu wa banja la nyumba ya Saulo, dzina lake ndiye Simei, mwana wa Gera; iyeyu anatulukako, nayenda natukwana.
Ndipo Simei, mwana wa Gera, Mbenjamini, wa ku Bahurimu, anafulumira natsika pamodzi ndi anthu a Yuda kuti akakomane ndi mfumu Davide.
Ndipo mwamuna wakeyo anapita naye, nanka nalira, namtsata kufikira ku Bahurimu. Pomwepo Abinere ananena naye, Choka, bwerera; ndipo anabwerera.