Husai nanena ndi Abisalomu, Iai; koma amene Yehova anasankha ndi anthu awa, ndi anthu onse a Israele, ine ndili wake, ndipo ndidzakhala naye iyeyu.
2 Samueli 16:17 - Buku Lopatulika Ndipo Abisalomu ananena ndi Husai, Kodi chimenechi ndi chifundo chako cha pa bwenzi lako? Unalekeranji kupita ndi bwenzi lako? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abisalomu ananena ndi Husai, Kodi chimenechi ndi chifundo chako cha pa bwenzi lako? Unalekeranji kupita ndi bwenzi lako? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Abisalomu adafunsa Husai kuti, “Kodi ndimo m'mene umamkondera bwenzi lako? Chifukwa chiyani sudapite naye limodzi bwenzi lakoyo?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abisalomu anafunsa Husai, “Kodi ichi ndi chikondi chimene ukumuonetsa bwenzi lako? Nʼchifukwa chiyani sunapite ndi bwenzi lako?” |
Husai nanena ndi Abisalomu, Iai; koma amene Yehova anasankha ndi anthu awa, ndi anthu onse a Israele, ine ndili wake, ndipo ndidzakhala naye iyeyu.
Ndipo kunali pakufika iye ku Yerusalemu kukakomana ndi mfumu, mfumu inanena naye, Chifukwa ninji sunapite nane Mefiboseti?
Kodi mubwezera Yehova chotero, anthu inu opusa ndi opanda nzeru? Kodi si ndiye Atate wanu, Mbuye wanu; anakulengani, nakukhazikitsani?