Koma Abisalomu anatumiza ozonda ku mafuko onse a Israele, kuti, Pakumva kulira kwa lipenga, pomwepo muzinena, Abisalomu ali mfumu ku Hebroni.
2 Samueli 15:9 - Buku Lopatulika Ndipo mfumu inanena naye, Muka ndi mtendere. Chomwecho ananyamuka, nanka ku Hebroni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mfumu inanena naye, Muka ndi mtendere. Chomwecho ananyamuka, nanka ku Hebroni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo mfumu idamuuza kuti, “Upite ndi mtendere.” Choncho Abisalomu adanyamuka napita ku Hebroni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mfumu inati kwa iye, “Pita mu mtendere” Kotero iye anapita ku Hebroni. |
Koma Abisalomu anatumiza ozonda ku mafuko onse a Israele, kuti, Pakumva kulira kwa lipenga, pomwepo muzinena, Abisalomu ali mfumu ku Hebroni.
Pakuti mnyamata wanu ndinawinda pakukhala ine ku Gesuri mu Aramu, ndi kuti, Yehova akadzandibwezeranso ndithu ku Yerusalemu, ine ndidzatumikira Yehova.
Ndipo Yoswa ndi Aisraele onse naye anakwera kuchokera ku Egiloni mpaka ku Hebroni, nauthira nkhondo;
Pamenepo Eli anayankha nati, Pita ndi mtendere; ndipo Mulungu wa Israele akupatse chopempha chako unachipempha kwa Iye.
Chomwecho Davide analandira m'dzanja lake zimene iye anamtengera; nanena naye, Ukwere kwanu mumtendere; ona, ndamvera mau ako, ndavomereza nkhope yako.