Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 15:5 - Buku Lopatulika

Ndipo kunatero kuti pakusendera munthu aliyense kudzamlambira, iye anatambasula dzanja lake, namgwira, nampsompsona.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo kunatero kuti pakusendera munthu aliyense kudzamlambira, iye anatambasula dzanja lake, namgwira, nampsompsona.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Choncho nthaŵi zonse munthu ankati akasendera pafupi kudzalambira Abisalomuyo, iye ankatambalitsa mkono, ndipo ankamgwira munthuyo namumpsompsona.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndipo nthawi zonse amati munthu akasendera pafupi ndi kumugwandira, Abisalomu amatambalitsa dzanja lake, kumuyimiritsa munthuyo ndi kupsompsona.

Onani mutuwo



2 Samueli 15:5
6 Mawu Ofanana  

Chomwecho Yowabu anadza kwa mfumu namuuza; ndipo pamene iye adaitana Abisalomu, iye anadza kwa mfumu naweramira nkhope yake pansi pamaso pa mfumu; ndipo mfumu inampsompsona Abisalomu.


Ndipo Yowabu ananena ndi Amasa, Uli bwino mbale wanga? Ndipo Yowabu anagwira ndevu za Amasa ndi dzanja lake lamanja kuti ampsompsone.


Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka, koma mumtima mwake munali nkhondo, mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga, koma anali malupanga osololasolola.


Pamene akometsa mau ake usamkhulupirire; pakuti m'mtima mwake muli zonyansa zisanu ndi ziwiri.


Sunandipatsa mpsompsono wa chibwenzi; koma uyu sanaleke kupsompsonetsa mapazi anga, chilowere muno Ine.