2 Samueli 15:29 - Buku Lopatulika Chifukwa chake Zadoki ndi Abiyatara ananyamulanso likasa la Mulungu nafika nalo ku Yerusalemu. Ndipo iwo anakhala kumeneko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake Zadoki ndi Abiyatara ananyamulanso likasa la Mulungu nafika nalo ku Yerusalemu. Ndipo iwo anakhala kumeneko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Zadoki ndi Abiyatara adanyamula Bokosi lija nabwerera nalo ku Yerusalemu, ndipo adakakhala kumeneko. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero Zadoki ndi Abiatara ananyamula Bokosi la Mulungu lija nabwerera nalo ku Yerusalemu, ndipo anakakhala kumeneko. |
Ndipo Davide anakwera pa chikweza cha ku Azitona nakwera nalira misozi; ndipo anafunda mutu wake nayenda ndi mapazi osavala; ndi anthu onse amene anali naye anafunda munthu yense mutu wake ndipo anakwera, nalira misozi pokwerapo.
Ndipo mfumu Davide anatumiza kwa Zadoki ndi Abiyatara ansembewo, nati, Mulankhule nao akulu a Yuda, kuti, Mukhale bwanji am'mbuyo kubwera nayo mfumu kunyumba yake? Pakuti mau a Aisraele onse anafika kwa mfumu akuti abwere nayo kunyumba yake.
Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu masiku a Abiyatara, mkulu wa ansembe, ndipo anadya mikate yoonetsera, yosaloleka kudya ena, koma ansembe okha, ndipo anawapatsanso iwo amene anali naye?