Pamenepo Abisalomu anaitana Yowabu kuti akamtumize iye kwa mfumu; koma anakana kubwera kwa iye; ndipo anamuitananso nthawi yachiwiri, koma anakana kubwera.
2 Samueli 14:30 - Buku Lopatulika Chifukwa chake iye anati kwa anyamata ake, Onani munda wa Yowabu uli pafupi ndi wanga, ndipo iye ali ndi barele pamenepo, mukani mukamtenthere. Ndipo anyamata a Abisalomu anatentha za m'mundawo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake iye anati kwa anyamata ake, Onani munda wa Yowabu uli pafupi ndi wanga, ndipo iye ali ndi barele pamenepo, mukani mukamtenthere. Ndipo anyamata a Abisalomu anatentha za m'mundawo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Abisalomu adauza atumiki ake kuti, “Munda wa Yowabu uli pafupi ndi wanga, ndipo ali ndi barele m'menemo. Pitani kautentheni.” Pompo atumiki a Abisalomu adapita kukautentha mundawo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Abisalomu anati kwa antchito ake, “Taonani, munda wa Yowabu uli pafupi ndi wanga ndipo muli barele mʼmenemo. Pitani mukawutenthe mundawo.” Ndipo antchito a Abisalomu anawutentha mundawo. |
Pamenepo Abisalomu anaitana Yowabu kuti akamtumize iye kwa mfumu; koma anakana kubwera kwa iye; ndipo anamuitananso nthawi yachiwiri, koma anakana kubwera.
Pamenepo Yowabu ananyamuka nafika kwa Abisalomu kunyumba yake, nanena naye, Chifukwa ninji anyamata anu anatentha za m'munda mwanga;
Pomwepo Yowabu anati, Sindiyenera kuchedwa nawe. Natenga mikondo itatu nagwaza nayo mtima wa Abisalomu alikukhala wamoyo pakati pa mtengowo.
Nati iye, Mgwetsereni pansi. Namgwetsera pansi, nuwazikako mwazi wake pakhoma ndi pa akavalo, nampondereza iye pansi.
Koma Samisoni, ananena nao, Nthawi ino ndikhala wosapalamula pa Afilisti, powachitira choipa ine.