Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 15:3 - Buku Lopatulika

3 Koma Samisoni, ananena nao, Nthawi ino ndikhala wosapalamula pa Afilisti, powachitira choipa ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Koma Samisoni, ananena nao, Nthawi yino ndikhala wosapalamula pa Afilisti, powachitira choipa ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Samisoni adaŵauza kuti, “Ulendo uno aliyense asandinene, ndikaŵachita choipa chachikulu Afilistiŵa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Samsoni anawawuza kuti, “Pano sindikhala wochimwa ndikawachita choyipa chachikulu Afilistiwa.”

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 15:3
5 Mawu Ofanana  

Chifukwa chake iye anati kwa anyamata ake, Onani munda wa Yowabu uli pafupi ndi wanga, ndipo iye ali ndi barele pamenepo, mukani mukamtenthere. Ndipo anyamata a Abisalomu anatentha za m'mundawo.


Koma kunali, tsiku lachisanu ndi chiwiri anati kwa mkazi wa Samisoni, Kopa mwamuna wako, atitanthauzire mwambiwo; tingatenthe iwe ndi nyumba ya atate wako ndi moto. Kodi mwatiitana kulanda zathu; si momwemo?


Koma atate wake ndi amai wake sanadziwe kuti chidachokera kwa Yehova ichi; popeza analikufuna kutola chifukwa ndi Afilisti. Ndipo nthawi ija Afilisti analamulira Israele.


Nati atate wake, Ndinanenetsa kuti umuda konse, potero ndinampereka kwa bwenzi lako; mng'ono wake sakoma koposa iye nanga? Ukhale naye, m'malo mwa winayu.


Namuka Samisoni, nagwira ankhandwe mazana atatu, natenga miuni, nalunza michira, naika muuni pakati pa michira iwiri iliyonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa