Nati iye, Mfumu mukumbukire Yehova Mulungu wanu kuti wolipsa mwazi asaonjeze kuononga, kuti angaononge mwana wanga. Niti iyo, Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la mwana wako lidzagwa pansi.
2 Samueli 14:21 - Buku Lopatulika Ndipo mfumuyo inanena ndi Yowabu, Taonanitu, ndachita chinthu ichi; chifukwa chake, pita nubwere nayenso mnyamatayo Abisalomu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mfumuyo inanena ndi Yowabu, Taonanitu, ndachita chinthu ichi; chifukwa chake, pita nubwere nayenso mnyamatayo Abisalomu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake mfumu idauza Yowabu kuti, “Chabwino tsono, ndavomera kuti zimenezi zichitike. Pita, kamtenge mnyamata uja Abisalomu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mfumu inati kwa Yowabu, “Chabwino, ine ndichita zimenezi. Pita kamutenge Abisalomuyo.” |
Nati iye, Mfumu mukumbukire Yehova Mulungu wanu kuti wolipsa mwazi asaonjeze kuononga, kuti angaononge mwana wanga. Niti iyo, Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la mwana wako lidzagwa pansi.
Ndipo Yowabu anagwa nkhope yake pansi, namlambira, nadalitsa mfumuyo; nati Yowabu, Lero mnyamata wanu ndadziwa kuti munandikomera mtima, mbuye wanga mfumu, popeza mfumu yachita chopempha mnyamata wake.
Ndipo mfumu inamva chisoni chachikulu; koma chifukwa cha malumbiro ake, ndi cha iwo akukhala pachakudya, sanafune kumkaniza.
Pakuti, pali Yehova wakupulumutsa Israele, chingakhale chili m'mwana wanga Yonatani, koma adzafa ndithu. Koma pakati pa anthu onse panalibe mmodzi wakumyankha iye.