Ndipo Natani ananena kwa Davide, Munthuyo ndi inu nomwe. Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Ndinakudzoza ukhale mfumu ya Israele, ndinakupulumutsa m'dzanja la Saulo;
2 Samueli 14:13 - Buku Lopatulika Ndipo mkaziyo anati, Chifukwa ninjinso munalingalira chinthu chotere pa anthu a Mulungu? Pakuti pakulankhula mau awa mfumu ikunga wopalamula, popeza mfumu siitumiza okamtenganso woingidwa wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mkaziyo anati, Chifukwa ninjinso munalingalira chinthu chotere pa anthu a Mulungu? Pakuti pakulankhula mau awa mfumu ikunga wopalamula, popeza mfumu siitumiza okamtenganso woingidwa wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo mkazi uja adafunsa kuti, “Chifukwa chiyani nanga mwaganiza zoŵachita zinthu zotere anthu a Mulungu? Chifukwatu pochita zimenezi inu amfumu mwadziimba mlandu nokha, malinga nkuti simudaitanitse wopirikitsidwa uja kuti abwererenso kwao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mkaziyo anati, “Nʼchiyani tsono chimene mwaganiza kuchitira zimenezi anthu a Mulungu? Pamene mfumu yanena izi, kodi sikudzitsutsa yokha, pakuti mfumu sinayitanitse mwana amene anamupirikitsa? |
Ndipo Natani ananena kwa Davide, Munthuyo ndi inu nomwe. Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Ndinakudzoza ukhale mfumu ya Israele, ndinakupulumutsa m'dzanja la Saulo;
Pamenepo mkaziyo anati, Mulole mdzakazi wanu alankhule mau kwa mbuye wanga mfumu. Niti iyo Nena.
Chifukwa chake tsono udzatero kwa mtumiki wanga Davide, Atero Yehova wa makamu, Ndinakuchotsa kubusako kumene unalikutsata nkhosa kuti udzakhale mfumu ya anthu anga, ndiwo Israele.
Ndipo akulu a anthu onse a mafuko onse a Israele anadziimika mu msonkhano wa anthu a Mulungu, anthu oyenda pansi zikwi mazana anai akusolola lupanga.