Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 7:8 - Buku Lopatulika

8 Chifukwa chake tsono udzatero kwa mtumiki wanga Davide, Atero Yehova wa makamu, Ndinakuchotsa kubusako kumene unalikutsata nkhosa kuti udzakhale mfumu ya anthu anga, ndiwo Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Chifukwa chake tsono udzatero kwa mtumiki wanga Davide, Atero Yehova wa makamu, Ndinakuchotsa kubusako kumene unalikutsata nkhosa kuti udzakhale mfumu ya anthu anga, ndiwo Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Nchifukwa chake tsono mtumiki wanga Davide umuuze kuti, Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, ndidakutenga kubusa kumene unkaŵeta nkhosa kuja kuti udzakhale mfumu yolamulira anthu anga Aisraele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 “Ndipo tsopano umuwuze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti: Ine ndinakutenga ku busa ukuweta nkhosa kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Aisraeli.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 7:8
17 Mawu Ofanana  

Ndipo Natani ananena kwa Davide, Munthuyo ndi inu nomwe. Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Ndinakudzoza ukhale mfumu ya Israele, ndinakupulumutsa m'dzanja la Saulo;


Ndipo mkaziyo anati, Chifukwa ninjinso munalingalira chinthu chotere pa anthu a Mulungu? Pakuti pakulankhula mau awa mfumu ikunga wopalamula, popeza mfumu siitumiza okamtenganso woingidwa wake.


Ndipo mau otsiriza a Davide ndi awa: Atero Davide mwana wa Yese, atero munthu wokwezedwa, ndiye wodzozedwa wa Mulungu wa Yakobo, ndi mwini nyimbo yokoma ya Israele.


Ndipo Davide analankhula ndi Yehova pamene anaona mthenga wakudwalitsa anthu, nati, Onani ndachimwa ine, ndinachita mwamphulupulu; koma nkhosa izi zinachitanji? Dzanja lanu likhale pa ine ndi pa nyumba ya atate wanga.


Masiku anapitawo, pamene Saulo anali mfumu yathu, inu ndinu amene munatsogolera Aisraele kutuluka nao ndi kubwera nao; ndipo Yehova ananena nanu, Uzidyetsa anthu anga Israele, ndi kukhala mtsogoleri wa Israele.


Koma Davide ananena ndi Mikala, Ndatero pamaso pa Yehova, amene anandisankha ine ndi kupitirira atate wako ndi banja lake lonse, nandiika ndikhale mtsogoleri wa anthu a Yehova, wa Israele, chifukwa chake ndidzasewera pamaso pa Yehova.


Ndipo Solomoni anati, Munamchitira mtumiki wanu Davide atate wanga zokoma zazikulu, monga umo anayenda pamaso panu ndi choonadi ndi chilungamo ndi mtima woongoka ndi Inu; ndipo mwamsungira chokoma ichi chachikulu kuti mwampatsa mwana kukhala pa mpando wake wachifumu monga lero lino.


Kuyambira tsiku lakutulutsa Ine anthu anga Aisraele m'dziko la Ejipito, sindinasankhe mzinda uliwonse mwa mafuko onse a Israele kumangamo nyumba yokhalamo dzina langa, koma ndinasankha Davide kukhala mfumu ya anthu anga Aisraele.


Chifukwa chake tsono, uzitero naye mtumiki wanga Davide, Atero Yehova wa makamu, Ndinakutenga kubusa potsata iwe nkhosa, kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Israele;


Ndipo Davide anati kwa Mulungu, Si ndine nanga ndalamulira kuti awerenge anthu? Inde, ndine amene ndachimwa ndi kuchita choipa ndithu; koma nkhosa izi zinachitanji? Dzanja lanu, Yehova Mulungu wanga, linditsutse ine ndi nyumba ya atate wanga, koma lisatsutse anthu anu ndi kuwachitira mliri.


ndipo Yehova ananditenga ndilikutsata nkhosa, nati kwa ine Yehova, Muka, nenera kwa anthu anga Israele.


amene anapeza chisomo pamaso pa Mulungu, napempha kuti apeze mokhalamo Mulungu wa Yakobo.


Pamenepo Samuele anatenga nsupa ya mafuta, nawatsanulira pamutu pake, nampsompsona iye, nati, Sanakudzozeni ndi Yehova kodi, Mukhale mfumu ya pa cholowa chake?


Amuutsa waumphawi m'fumbi, nanyamula wosowa padzala, kukamkhalitsa kwa akalonga; ndi kuti akhale nacho cholowa cha chimpando cha ulemerero. Chifukwa nsanamira za dziko lapansi nza Yehova, ndipo Iye anakhazika dziko pa izo.


Mawa, monga dzuwa lino, ndidzakutumizira munthu wochokera ku dziko la Benjamini, udzamdzoza iye akhale mtsogoleri wa anthu anga Israele, kuti akawapulumutse anthu anga m'manja a Afilisti; pakuti Ine ndinapenya pa anthu anga, popeza kulira kwao kunandifika Ine.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa