2 Samueli 7:8 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 “Ndipo tsopano umuwuze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti: Ine ndinakutenga ku busa ukuweta nkhosa kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Aisraeli. Onani mutuwoBuku Lopatulika8 Chifukwa chake tsono udzatero kwa mtumiki wanga Davide, Atero Yehova wa makamu, Ndinakuchotsa kubusako kumene unalikutsata nkhosa kuti udzakhale mfumu ya anthu anga, ndiwo Israele. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Chifukwa chake tsono udzatero kwa mtumiki wanga Davide, Atero Yehova wa makamu, Ndinakuchotsa kubusako kumene unalikutsata nkhosa kuti udzakhale mfumu ya anthu anga, ndiwo Israele. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Nchifukwa chake tsono mtumiki wanga Davide umuuze kuti, Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, ndidakutenga kubusa kumene unkaŵeta nkhosa kuja kuti udzakhale mfumu yolamulira anthu anga Aisraele. Onani mutuwo |
Solomoni anayankha kuti, “Inu munaonetsa kukoma mtima kwanu kwakukulu kwa kapolo wanu, abambo anga Davide, chifukwa anali wokhulupirika pamaso panu, wolungama mtima ndiponso wa mtima wangwiro. Inu mukupitirizabe kukoma mtima kwanu kwakukulu kwa iye ndipo mwamupatsa mwana kuti akhale pa mpando wake waufumu lero lino.
Davide anati kwa Mulungu, “Kodi si ine amene ndinalamula kuti ankhondo awerengedwe? Ine mʼbusa ndi amene ndachimwa, ndiye ndachita zoyipa. Anthuwa ali ngati nkhosa zosalakwa. Kodi iwowa achita chiyani? Inu Yehova Mulungu wanga, langani ineyo pamodzi ndi banja langa, koma musalole kuti mliriwu ukhale pa anthu anuwa.”
Ndipo Samueli anatenga botolo la mafuta nathira mafutawo pa mutu wa Sauli ndipo anapsompsona nati, “Yehova wakudzoza kuti ukhale mtsogoleri wa anthu ake, Aisraeli. Iwe udzalamulira anthu a Yehova ndiponso udzawapulumutsa mʼmanja mwa adani awo owazungulira. Chizindikiro chakuti Yehova wakudzoza kuti ukhale mtsogoleri wa anthu ake ndi ichi: