Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 13:8 - Buku Lopatulika

Chomwecho Tamara anapita kunyumba ya mlongo wake Aminoni; ndipo iye anali chigonere. Ndipo anatenga ufa naukanda naumba timitanda pamaso pake, nakazinga timitandato.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Chomwecho Tamara anapita kunyumba ya mlongo wake Aminoni; ndipo iye anali chigonere. Ndipo anatenga ufa naukanda naumba timitanda pamaso pake, nakazinga timitandato.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tamara adapitadi kunyumba kwa mbale wake Aminoni ku malo kumene ankagona. Adatenga ufa, naukanda, naumba makeke, Aminoniyo akupenya, ndipo adaphika makekewo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Choncho Tamara anapitadi ku nyumba ya mlongo wake Amnoni kumalo kumene ankagona. Anakanda ufa, nawumba buledi Amunoniyo akuona ndipo anaphika bulediyo.

Onani mutuwo



2 Samueli 13:8
4 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anatumiza mau kwao kwa Tamara, kuti, Upite kunyumba ya mlongo wako Aminoni, numkonzere chakudya.


Ndipo anatenga chiwaya natitulutsa pamaso pake; koma anakana kudya. Ndipo Aminoni anati, Anthu onse atuluke kundisiya ine. Natuluka onse, kumsiya.


Wotembereredwa iye wakugona ndi mlongo wake, mwana wamkazi wa atate wake, kapena mwana wamkazi wa make. Ndi anthu onse anene, Amen.


Ndipo mkaziyo anali ndi mwanawang'ombe wonenepa m'nyumbamo; ndipo anafulumira, namupha, natenga ufa naukanyanga mkate wopanda chotupitsa;