Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 13:8 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Choncho Tamara anapitadi ku nyumba ya mlongo wake Amnoni kumalo kumene ankagona. Anakanda ufa, nawumba buledi Amunoniyo akuona ndipo anaphika bulediyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

8 Chomwecho Tamara anapita kunyumba ya mlongo wake Aminoni; ndipo iye anali chigonere. Ndipo anatenga ufa naukanda naumba timitanda pamaso pake, nakazinga timitandato.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Chomwecho Tamara anapita kunyumba ya mlongo wake Aminoni; ndipo iye anali chigonere. Ndipo anatenga ufa naukanda naumba timitanda pamaso pake, nakazinga timitandato.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Tamara adapitadi kunyumba kwa mbale wake Aminoni ku malo kumene ankagona. Adatenga ufa, naukanda, naumba makeke, Aminoniyo akupenya, ndipo adaphika makekewo.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 13:8
4 Mawu Ofanana  

Davide anatumiza mawu kwa Tamara ku nyumba yaufumu kuti, “Pita ku nyumba ya mlongo wako Amnoni ndipo ukamukonzere chakudya.”


Kenaka iye anatenga chiwaya ndipo anamupatsa bulediyo, koma iyeyo anakana. Amnoni anati “Uza aliyense atuluke muno.” Ndipo aliyense anatuluka.


“Ndi wotembereredwa munthu amene agonana ndi mlongo wake, mwana wamkazi wa abambo ake kapena mwana wamkazi wa amayi ake.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”


Mkaziyo anali ndi mwana wangʼombe wonenepa ndipo anamupha mwachangu. Anatenga ufa nawukanyanga ndipo anaphika buledi wopanda yisiti.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa