Ndipo Rubeni anabwera kudzenje, ndipo taonani, Yosefe mulibe m'dzenjemo: ndipo iye anang'amba nsalu yake.
2 Samueli 13:31 - Buku Lopatulika Pamenepo mfumu inanyamuka ning'amba zovala zake nigona pansi, ndipo anyamata ake onse anaimirirapo ndi zovala zao zong'ambika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo mfumu inanyamuka ning'amba zovala zake nigona pansi, ndipo anyamata ake onse anaimirirapo ndi zovala zao zong'ambika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pompo mfumu idadzuka, ning'amba zovala zake, nkudzigwetsa pansi. Atumiki ake onse amene anali pafupi naye, nawonso adang'amba zovala zao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mfumu inayimirira, ningʼamba zovala zake ndi kugona pa dothi. Antchito ake onse anayimirira pomwepo atangʼamba zovala zawo. |
Ndipo Rubeni anabwera kudzenje, ndipo taonani, Yosefe mulibe m'dzenjemo: ndipo iye anang'amba nsalu yake.
Yakobo ndipo anang'amba malaya ake, na vala chiguduli m'chuuno mwake namlirira mwana wake masiku ambiri.
Chifukwa chake Davide anapempherera mwanayo kwa Mulungu; Davide nasala kudya, nalowa, nagona usiku wonse pansi.
Ndipo kunali akali panjira, mau anafika kwa Davide, kuti, Abisalomu anapha ana aamuna onse a mfumu, osatsalapo ndi mmodzi yense.
Ndipo Davide anati kwa Yowabu ndi kwa anthu onse okhala naye, Ng'ambani zovala zanu, ndi kudzimangira ziguduli m'chuuno, nimulire Abinere. Ndipo mfumu Davide anatsata chithatha.
Pamenepo Yobu ananyamuka, nang'amba malaya ake, nameta mutu wake, nagwa pansi, nalambira,
Ndipo Yoswa anang'amba zovala zake, nagwa nkhope yake pansi, ku likasa la Yehova, mpaka madzulo, iye ndi akuluakulu a Israele, nathira fumbi pamitu pao.