Atatero Aminoni anadana naye ndi chidani chachikulu kopambana; pakuti chidani chimene anamuda nacho, chinali chachikulu koposa chikondi adamkonda nacho. Ndipo Aminoni ananena naye, Nyamuka, choka.
2 Samueli 13:16 - Buku Lopatulika Koma iye ananena naye, Usamatero, pakuti choipa ichi chakuti ulikundipirikitsa nchachikulu choposa china chija unandichitira ine. Koma anakana kumvera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma iye ananena naye, Usamatero, pakuti choipa ichi chakuti ulikundipirikitsa nchachikulu choposa china chija unandichitira ine. Koma anakana kumvera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Tamarayo adati, “Iyai, mlongo wanga, kundipirikitsa chotere nkulakwa koposa zimene wandichitazi.” Koma Aminoni sadafune kumva zimene ankanena Tamarazo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anayankha, “Ayi! Kundithamangitsa kukhala kulakwa kwakukulu kuposa zimene wachita kale kwa ine.” Koma anakana kumumvera. |
Atatero Aminoni anadana naye ndi chidani chachikulu kopambana; pakuti chidani chimene anamuda nacho, chinali chachikulu koposa chikondi adamkonda nacho. Ndipo Aminoni ananena naye, Nyamuka, choka.
Pomwepo anaitana mnyamata wake amene anamtumikira, nati, Tulutsa mkazi uyu kwa ine, nupiringidze chitseko atapita iye.