Ndipo panali zitapita izi, kuti mkazi wa mbuyake anamyang'anira maso Yosefe: ndipo mkaziyo anati, Gona ndi ine.
2 Samueli 13:11 - Buku Lopatulika Ndipo pamene anabwera nato pafupi kuti adye, iye anamgwira, nanena naye, Idza nugone nane, mlongo wanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene anabwera nato pafupi kuti adye, iye anamgwira, nanena naye, Idza nugone nane, mlongo wanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma atafika nacho chakudyacho pafupi ndi Aminoni kuti adye, Aminoni adamgwira Tamara, namuuza kuti, “Bwera ugone nane, iwe Tamara.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma atabweretsa kwa iye kuti adye, anamugwira ndipo anati, “Bwera ugone nane, iwe mlongo wanga.” |
Ndipo panali zitapita izi, kuti mkazi wa mbuyake anamyang'anira maso Yosefe: ndipo mkaziyo anati, Gona ndi ine.
Ndipo Aminoni anati kwa Tamara, Bwera nacho chakudya kuchipinda kuti ndikadye cha m'manja mwako. Ndipo Tamara anatenga timitanda anatipangato, nabwera nato kuchipinda kwa Aminoni mlongo wake.
Ndipo wina anachita chonyansa ndi mkazi wa mnansi wake, winanso wadetsa mpongozi wake mwamanyazi, ndi wina mwa iwe anaipitsa mlongo wake mwana wamkazi wa atate wake.