Chomwecho iwo anayalira Abisalomu hema pamwamba pa nyumba; ndipo Abisalomu analowa kwa akazi aang'ono a atate wake pamaso pa Aisraele onse.
2 Samueli 12:12 - Buku Lopatulika Pakuti iwe unachichita m'tseri; koma Ine ndidzachita chinthu ichi pamaso pa Aisraele onse, dzuwa lili nde. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti iwe unachichita m'tseri; koma Ine ndidzachita chinthu ichi pamaso pa Aisraele onse, dzuwa lili nde. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwe unkachita zimenezo m'seri, koma Ine ndidzazichita pamaso pa Aisraele onse, masana ndithu.’ ” Apo Davide adauza Natani kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwe unachita zimenezi mwamseri koma Ine ndidzachita izi masanasana Aisraeli onse akuona.’ ” |
Chomwecho iwo anayalira Abisalomu hema pamwamba pa nyumba; ndipo Abisalomu analowa kwa akazi aang'ono a atate wake pamaso pa Aisraele onse.
Pakuti Mulungu adzanena mlandu wa zochita zonse, ndi zobisika zonse, ngakhale zabwino ngakhale zoipa.
Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.