Ndipo anati kwa iwo, Kodi ali bwino? Nati, Ali bwino: taonani, Rakele mwana wake wamkazi alinkudza nazo nkhosa.
2 Samueli 11:7 - Buku Lopatulika Ndipo pakufika kwa iye Uriya uja, Davide anamfunsa kuti, Yowabu ali bwanji? Ndi anthu ali bwanji? Ndi nkhondo ili bwanji? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pakufika kwa iye Uriya uja, Davide anamfunsa kuti, Yowabu ali bwanji? Ndi anthu ali bwanji? Ndi nkhondo ili bwanji? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Uriya atabwera, Davide adamufunsa m'mene analiri Yowabu kunkhondoko, ndiponso m'mene analiri anthu, ndi m'menenso nkhondo inkayendera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Uriya atafika kwa Davide, Davide anamufunsa za momwe analili Yowabu, za asilikali ndi momwe nkhondo inkayendera. |
Ndipo anati kwa iwo, Kodi ali bwino? Nati, Ali bwino: taonani, Rakele mwana wake wamkazi alinkudza nazo nkhosa.
Ndipo anati kwa iye, Pita tsopano, nukaone ngati abale ako ali bwino, ndi ngati zoweta zili bwino; nundibwezere ine mau. Ndipo anamtuma iye kuchokera m'chigwa cha Hebroni, ndipo anadza ku Sekemu.
Davide natumiza kwa Yowabu, nati, Unditumizire Uriya Muhiti. Ndipo Yowabu anatumiza Uriya kwa Davide.
Ndipo Mose anatuluka kukakomana ndi mpongozi wake, nawerama, nampsompsona; nafunsana ali bwanji, nalowa m'hema.
Ndipo Davide anasiya akatundu ake m'dzanja la wosungira akatundu, nathamangira ku khamulo, nadza nawalonjera abale ake.