Ndipo akuponyawo amene anali palinga anaponya anyamata anu; ndipo anyamata ena a mfumu anafa, ndi mnyamata wanu Uriya Muhiti, iyenso anafa.
2 Samueli 11:25 - Buku Lopatulika Pomwepo Davide ananena ndi mthengawo, Udzatero kwa Yowabu, Chisakuipire ichi, lupanga limaononga wina ndi mnzake. Onjeza kulimbitsa nkhondo yako pamzindapo, nuupasule; numlimbikitse motere. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo Davide ananena ndi mthengawo, Udzatero kwa Yowabu, Chisakuipire ichi, lupanga limaononga wina ndi mnzake. Onjeza kulimbitsa nkhondo yako pamudzipo, nuupasule; numlimbikitse motere. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Davide adauza wamthenga uja kuti, “Kamuuze Yowabu kuti, ‘Zimenezi usavutike nazo, poti wakufa sadziŵika. Ulimbike polimbana ndi mzindawo, ndi kuugonjetsa.’ Choncho ukamlimbitse mtima Yowabuyo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide anamuwuza mthengayo kuti, “Ukanene izi kwa Yowabu: ‘Zimenezi zisakukhumudwitse; lupanga limapha wina nthawi zinanso wina. Limbikitsa nkhondo pa mzindawo ndipo uwuwononge!’ Ukanene zimenezi pomulimbikitsa Yowabu.” |
Ndipo akuponyawo amene anali palinga anaponya anyamata anu; ndipo anyamata ena a mfumu anafa, ndi mnyamata wanu Uriya Muhiti, iyenso anafa.
Ndipo pamene mkazi wa Uriya anamva kuti Uriya mwamuna wake adamwalira, iye analira maliro a mwamuna wake.
Koma anthu, ndiwo amuna a Israele, anadzilimbitsa nanikanso nkhondo kumene anandandalika tsiku loyambalo.
Ndipo muyang'anire, ngati likwera panjira ya malire akeake ku Betesemesi, Iye anatichitira choipa ichi chachikulu; koma likapanda kutero, tidzadziwapo kuti dzanja limene linatikantha, silili lake; langotigwera tsokali.