Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 11:24 - Buku Lopatulika

Ndipo akuponyawo amene anali palinga anaponya anyamata anu; ndipo anyamata ena a mfumu anafa, ndi mnyamata wanu Uriya Muhiti, iyenso anafa.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo akuponyawo amene anali palinga anaponya anyamata anu; ndipo anyamata ena a mfumu anafa, ndi mnyamata wanu Uriya Muhiti, iyenso anafa.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono anthu oponya mivi ankalasa ankhondo anu kuchokera m'linga. Ndipo ankhondo ena mwa ankhondo a inu mfumu adaphedwa. Wankhondo wanu uja, Uriya Muhiti, nayenso adaphedwa.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndipo anthu oponya mivi anatiponyera kuchokera pa khoma, anthu ena a mfumu afa. Kuwonjezera apo, mtumiki wanu Uriya Mhiti wafanso.”

Onani mutuwo



2 Samueli 11:24
4 Mawu Ofanana  

Ndipo mthengawo unati kwa Davide, Anthuwo anatipambana natulukira kwa ife kumundako, koma tinawagwera kufikira polowera kuchipata.


Pomwepo Davide ananena ndi mthengawo, Udzatero kwa Yowabu, Chisakuipire ichi, lupanga limaononga wina ndi mnzake. Onjeza kulimbitsa nkhondo yako pamzindapo, nuupasule; numlimbikitse motere.


Tinawagwetsa; Hesiboni waonongeka kufikira ku Diboni, ndipo tinawapululutsa kufikira ku Nofa. Ndiwo wakufikira ku Medeba.


Pamenepo Davide anayankha nati kwa Ahimeleki Muhiti, ndi Abisai, mwana wa Zeruya, mbale wake wa Yowabu, nati, Adzatsikira nane ndani kumisasako kwa Saulo? Nati Abisai, Nditsika nanu ndine.