Koma Uriya anagona pa khomo la nyumba ya mfumu pamodzi ndi anyamata onse a mbuye wake, osatsikira kunyumba yake.
2 Samueli 11:13 - Buku Lopatulika Ndipo pakumuitana Davide, iyeyo anadya namwa pamaso pake; Davide namledzeretsa; ndipo usiku anatuluka kukagona pa kama wake pamodzi ndi anyamata a mbuye wake; koma sanatsikire kunyumba yake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pakumuitana Davide, iyeyo anadya namwa pamaso pake; Davide namledzeretsa; ndipo usiku anatuluka kukagona pa kama wake pamodzi ndi anyamata a mbuye wake; koma sanatsikire kunyumba yake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Davide adaitana Uriya, nadya naye ndipo adamwa kwambiri, kotero kuti Davide adamledzeretsa. Komabe madzulo Uriya adapita kukagona pogona pake, pamodzi ndi antchito a mfumu, osapita kunyumba kwake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide anayitana Uriya nadya ndi kumwa naye, ndipo Davide anamuledzeretsa. Koma madzulo Uriya anapita kukagona pa mphasa pamodzi ndi antchito a mbuye wake. Iye sanapite ku nyumba yake. |
Koma Uriya anagona pa khomo la nyumba ya mfumu pamodzi ndi anyamata onse a mbuye wake, osatsikira kunyumba yake.
Pomwepo Abisalomu anati, Ngati nkutero, mulole mbale wanga Aminoni apite nafe. Ndipo mfumu inanena naye, Iye apitirenji nawe?
Ndipo Mose anati kwa Aroni, Anthu awa anakuchitiranji, kuti iwe watengera iwo kulakwa kwakukulu kotere?
Ndani ali ndi chisoni? Ndani asauka? Ndani ali ndi makangano? Ndani ang'ung'udza? Ndani alasidwa chabe? Ndani afiira maso?
Tsoka wakuninkha mnzake chakumwa, ndi kuonjezako mankhwala ako, ndi kumledzeretsa, kuti upenyerere manyazi ao!