Ndipo pakumuitana Davide, iyeyo anadya namwa pamaso pake; Davide namledzeretsa; ndipo usiku anatuluka kukagona pa kama wake pamodzi ndi anyamata a mbuye wake; koma sanatsikire kunyumba yake.
2 Samueli 11:12 - Buku Lopatulika Ndipo Davide anati kwa Uriya, Utsotse pano leronso, ndipo mawa ndidzakulola umuke. Chomwecho Uriya anakhala ku Yerusalemu tsiku lomwelo ndi m'mawa mwake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anati kwa Uriya, Utsotse pano leronso, ndipo mawa ndidzakulola umuke. Chomwecho Uriya anakhala ku Yerusalemu tsiku lomwelo ndi m'mawa mwake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Davide adauza Uriya kuti, “Utandale pompano lero, maŵa ndikulola kuti uzipita.” Choncho Uriya adatandala ku Yerusalemu tsiku limenelo mpaka m'maŵa mwake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Davide anati kwa iye, “Ukhale konkuno tsiku lina limodzi, ndipo mawa ndikulola kuti upite.” Kotero Uriya anakhala mu Yerusalemu tsiku limenelo ndi tsiku linalo. |
Ndipo pakumuitana Davide, iyeyo anadya namwa pamaso pake; Davide namledzeretsa; ndipo usiku anatuluka kukagona pa kama wake pamodzi ndi anyamata a mbuye wake; koma sanatsikire kunyumba yake.
Koma udzatuluka kwa iyenso, manja ako pamutu pako; pakuti Yehova wakana zokhulupirira zako, ndipo sudzapindula m'menemo.