Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 11:12 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Ndipo Davide anati kwa iye, “Ukhale konkuno tsiku lina limodzi, ndipo mawa ndikulola kuti upite.” Kotero Uriya anakhala mu Yerusalemu tsiku limenelo ndi tsiku linalo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

12 Ndipo Davide anati kwa Uriya, Utsotse pano leronso, ndipo mawa ndidzakulola umuke. Chomwecho Uriya anakhala ku Yerusalemu tsiku lomwelo ndi m'mawa mwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo Davide anati kwa Uriya, Utsotse pano leronso, ndipo mawa ndidzakulola umuke. Chomwecho Uriya anakhala ku Yerusalemu tsiku lomwelo ndi m'mawa mwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Apo Davide adauza Uriya kuti, “Utandale pompano lero, maŵa ndikulola kuti uzipita.” Choncho Uriya adatandala ku Yerusalemu tsiku limenelo mpaka m'maŵa mwake.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 11:12
4 Mawu Ofanana  

Davide anayitana Uriya nadya ndi kumwa naye, ndipo Davide anamuledzeretsa. Koma madzulo Uriya anapita kukagona pa mphasa pamodzi ndi antchito a mbuye wake. Iye sanapite ku nyumba yake.


“Ngakhale zoyipa zili zozuna mʼkamwa mwake ndipo amazibisa kunsi kwa lilime lake,


Mudzachokanso kumeneko manja ali kunkhongo. Popeza Ine Yehova ndawakana anthu amene munkawadalira, choncho sadzakuthandizani konse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa