2 Samueli 11:10 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene anauza Davide kuti, Uriya sanatsikire kunyumba yake, Davide ananena ndi Uriya, Kodi sunabwere kuulendo? Chifukwa ninji sunatsikire kunyumba yako?
Onani mutuwo
Ndipo pamene anauza Davide kuti, Uriya sanatsikire kunyumba yake, Davide ananena ndi Uriya, Kodi sunabwera kuulendo? Chifukwa ninji sunatsikira kunyumba yako?
Onani mutuwo
Tsono anthu adamuuza Davide kuti, “Uriyatu sadapite kunyumba kwake.” Davideyo adafunsa Uriya kuti, “Kodi suja iwe wachokera ku ulendo? Nanga bwanji sudapite kunyumba kwako?”
Onani mutuwo
Davide atawuzidwa kuti, “Uriya sanapite ku nyumba yake.” Iye anafunsa kuti, “Kodi iwe sunachokera kutali? Nʼchifukwa chiyani sunapite ku nyumba yako?”
Onani mutuwo