Ndipo pakufika Aaramu a ku Damasiko kudzathandiza Hadadezere mfumu ya ku Zoba, Davide anakanthako Aaramu zikwi makumi awiri mphambu ziwiri.
2 Samueli 10:13 - Buku Lopatulika Chomwecho Yowabu ndi anthu amene anali naye anayandikira kuponyana nkhondo ndi Aaramu. Ndipo iwowa anathawa pamaso pake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chomwecho Yowabu ndi anthu amene anali naye anayandikira kuponyana nkhondo ndi Aaramu. Ndipo iwowa anathawa pamaso pake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Yowabu ndi anthu ake adasendera pafupi ndi Asiriya aja kuti amenyane nawo nkhondo, koma Asiriyawo adathaŵa iye akufika. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Yowabu ndi ankhondo amene anali naye anapita kukamenyana ndi Aaramu, ndipo iwo anathawa pamaso pake. |
Ndipo pakufika Aaramu a ku Damasiko kudzathandiza Hadadezere mfumu ya ku Zoba, Davide anakanthako Aaramu zikwi makumi awiri mphambu ziwiri.
Muwachotse monga utsi uchotseka; monga phula lisungunuka pamoto, aonongeke oipa pamaso pa Mulungu.