Yuda, abale ako adzakuyamika iwe; dzanja lako lidzakhala pa khosi la adani ako; ana aamuna a atate wako adzakuweramira.
2 Samueli 1:18 - Buku Lopatulika nawauza aphunzitse ana Ayuda nyimbo iyi ya Uta, onani inalembedwa m'buku la Yasara, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nawauza aphunzitse ana Ayuda nyimbo iyi ya Uta, onani inalembedwa m'buku la Yasara, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo adalamula kuti mau a madandaulowo aŵaphunzitse kwa anthu a ku Yuda. Mau ake ndi aŵa, monga adalembedwera m'buku la Yasara. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo analamula kuti anthu a ku Yuda aphunzitsidwe nyimbo ya maliroyi imene yalembedwa mʼbuku la Yasari: |
Yuda, abale ako adzakuyamika iwe; dzanja lako lidzakhala pa khosi la adani ako; ana aamuna a atate wako adzakuweramira.
Tsikuli munaima pamaso pa Yehova Mulungu wanu mu Horebu muja Yehova anati kwa ine, Ndisonkhanitsire anthu, ndidzawamvetsa mau anga, kuti aphunzire kundiopa Ine masiku ao onse akukhala ndi moyo padziko lapansi, ndi kuti aphunzitse ana ao.
Ndipo dzuwa linalinda, ndi mwezi unaima mpaka anthu adabwezera chilango adani ao. Kodi ichi sichilembedwa m'buku la Yasara? Ndipo dzuwa linakhala pakati pa thambo, losafulumira kulowa ngati tsiku lamphumphu.