Ndipo pamene Mose anaona kuti anthu anamasuka, popeza Aroni adawamasula kuti awatonze adani ao,
2 Akorinto 5:3 - Buku Lopatulika ngatitu povekedwa sitidzapezedwa amaliseche. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ngatitu povekedwa sitidzapezedwa amaliseche. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa kuti titaivala, tisadzapezeke amaliseche. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero chifukwa tikavala, sitidzapezekanso amaliseche. |
Ndipo pamene Mose anaona kuti anthu anamasuka, popeza Aroni adawamasula kuti awatonze adani ao,
Pakutinso m'menemo tibuula, ndi kukhumbitsa kuvekedwa ndi chokhalamo chathu chochokera Kumwamba;
Pakutinso ife okhala mu msasawu tibuula, pothodwa; si kunena kuti tifuna kuvulidwa, koma kuvekedwa, kuti chaimfacho chimezedwe ndi moyo.
(Taonani, ndidza ngati mbala. Wodala iye amene adikira, nasunga zovala zake, kuti angayende wausiwa, nangapenye anthu usiwa wake.)
ndikulangiza ugule kwa Ine golide woyengeka m'moto, kuti ukakhale wachuma, ndi zovala zoyera, kuti ukadziveke, ndi kuti manyazi a usiwa wako asaoneke; ndi mankhwala opaka m'maso mwako, kuti ukaone.