Poyamba, ndiyamika Mulungu wanga mwa Yesu Khristu chifukwa cha inu nonse, chifukwa kuti mbiri ya chikhulupiriro chanu idamveka padziko lonse lapansi.
2 Akorinto 3:2 - Buku Lopatulika Inu ndinu kalata yathu, wolembedwa mu mitima yathu, wodziwika ndi wowerengedwa ndi anthu onse; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Inu ndinu kalata wathu, wolembedwa mu mitima yathu, wodziwika ndi wowerengedwa ndi anthu onse; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kalata yotichitira umboniyo ndinu nomwe. Idalembedwa m'mitima mwathu, kuti anthu onse aidziŵe ndi kumaiŵerenga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu ndinu kalata yathu, yolembedwa pa mitima yathu, yodziwika ndi yowerengedwa ndi aliyense. |
Poyamba, ndiyamika Mulungu wanga mwa Yesu Khristu chifukwa cha inu nonse, chifukwa kuti mbiri ya chikhulupiriro chanu idamveka padziko lonse lapansi.
Monga mwa chisomo cha Mulungu chidapatsidwa kwa ine, ngati mwini mamangidwe waluso, ndinaika maziko, koma wina amangapo. Koma yense ayang'anire umo amangira pamenepo.
Ndipo ndidzapereka ndi kuperekedwa konse chifukwa cha miyoyo yanu mokondweratu. Ngati ndikonda inu kochuluka koposa, kodi ndikondedwa kochepa?
Kodi tilikuyambanso kudzivomereza tokha? Kapena kodi tisowa, monga ena, makalata otivomerezetsa kwa inu, kapena ochokera kwa inu?
Sindinena ichi kuti ndikutsutseni: pakuti ndanena kale kuti muli mu mitima yathu, kuti tife limodzi ndi kukhala ndi moyo limodzi.
monga kundiyenera ine kuyesa za inu nonse, popeza ndili nako m'mtima mwanga, kuti inu m'zomangira zanga, ndipo m'chodzikanira, ndi matsimikizidwe a Uthenga Wabwino, inu nonse muli oyanjana nane m'chisomo.
Pakuti kutuluka kwa inu kudamveka mau a Ambuye, osati mu Masedoniya ndi Akaya mokha, komatu m'malo monse chikhulupiriro chanu cha kwa Mulungu chidatuluka; kotero kuti sikufunika kwa ife kulankhula kanthu.