2 Akorinto 2:4 - Buku Lopatulika Pakuti m'chisautso chambiri ndi kuwawa mtima ndinalembera inu ndi misozi yambiri; si kuti ndikumvetseni chisoni, koma kuti mukadziwe chikondi cha kwa inu, chimene ndili nacho koposa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti m'chisautso chambiri ndi kuwawa mtima ndinalembera inu ndi misozi yambiri; si kuti ndikumvetseni chisoni, koma kuti mukadziwe chikondi cha kwa inu, chimene ndili nacho koposa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene ndidakulemberani kalata ija, mtima wanga unali wovutika ndi wopsinjika ndithu, ndipo ndinkalira misozi. Sindidafune kukupweteketsani mtima, koma makamaka ndinkafuna kuti mudziŵe kuti ndimakukondani kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti ndinakulemberani kalata ija ndili wopsinjika ndi wowawidwa mtima kwambiri ndi kutuluka misozi yambiri, osati pofuna kukumvetsani chisoni koma kuti ndikudziwitseni kuti ndimakukondani kwambiri. |
Pakuti ndichita nsanje pa inu ndi nsanje ya Mulungu; pakuti ndinakupalitsani ubwenzi mwamuna mmodzi, kuti ndikalangize inu ngati namwali woyera mtima kwa Khristu.
Ndipo ndidzapereka ndi kuperekedwa konse chifukwa cha miyoyo yanu mokondweratu. Ngati ndikonda inu kochuluka koposa, kodi ndikondedwa kochepa?
Pakuti chifukwa cha ichi ndalembanso, kuti ndidziwe mayesedwe anu, ngati muli omvera m'zonse.
Chifukwa chake ndingakhale ndalembera kwa inu, sindinachita chifukwa cha iye amene anachita choipa, kapena chifukwa cha iye amene anachitidwa choipa, koma kuti khama lanu la kwa ife lionetsedwe kwa inu pamaso pa Mulungu.
Pakuti ambiri amayenda, za amene ndinakuuzani kawirikawiri, ndipo tsopanonso ndikuuzani ndi kulira, ali adani a mtanda wa Khristu;