Ndipo Mikaya anati, Mukabwera ndithu ndi mtendere Yehova sanalankhule mwa ine. Nati, Mvetsani, anthu inu nonse.
2 Akorinto 13:8 - Buku Lopatulika Pakuti sitikhoza kanthu pokana choonadi, koma povomereza choonadi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti sitikhoza kanthu pokana choonadi, koma povomereza choonadi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakuti sitingathe kuchita chilichonse chotsutsana ndi choona, koma zokhazokha zothandizira choonacho. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti sitingachite chilichonse chotsutsana ndi choonadi, koma chokhacho chovomerezana ndi choonadi. |
Ndipo Mikaya anati, Mukabwera ndithu ndi mtendere Yehova sanalankhule mwa ine. Nati, Mvetsani, anthu inu nonse.
Monga mpheta ilikuzungulira, ndi namzeze alikuuluka, momwemo temberero la pachabe silifikira.
Koma Yesu anati, Musamamletsa iye; pakuti palibe munthu adzachita champhamvu m'dzina langa, nadzakhoza msanga kundinenera Ine zoipa.
Pakuti ndingakhale ndikadzitamandira kanthu kochulukira za ulamuliro (umene anatipatsa Ambuye kukumangirira, ndipo si kukugwetsera kwanu), sindidzanyazitsidwa;
Chifukwa cha ichi ndilembera izi pokhala palibe ine, kuti pokhala ndili pomwepo ndingachite mowawitsa, monga mwa ulamuliro umene Ambuye anandipatsa ine wakumangirira, ndipo si wakugwetsa.
Ndipo tipemphera Mulungu kuti musachite kanthu koipa; sikuti ife tikaoneke ovomerezeka, koma kuti inu mukachite chabwino, tingakhale ife tikhala monga osatsimikizidwa.
Pakuti tikondwera, pamene ife tifooka ndi inu muli amphamvu; ichinso tipempherera, ndicho ungwiro wanu.
a iwo ali Himeneo ndi Aleksandro, amene ndawapereka kwa Satana, kuti aphunzire kusalankhula zamwano.