Pakuti, makalatatu, ati, ndiwo olemera, ndi amphamvu; koma maonekedwe a thupi lake ngofooka, ndi mau ake ngachabe.
2 Akorinto 10:11 - Buku Lopatulika Woteroyo ayese ichi kuti monga tili ife ndi mau mwa makalata, pokhala palibe ife, tili oterenso m'machitidwe pokhala tili pomwepo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Woteroyo ayese ichi kuti monga tili ife ndi mau mwa akalata, pokhala palibe ife, tili oterenso m'machitidwe pokhala tili pomwepo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu oganiza zotere, adziŵe kuti palibe kusiyana pakati pa zimene timanena m'makalata pamene tili nanu kutali ndi zimene timachita tikakhala nanu pamodzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu oterewa ayenera kuzindikira kuti zomwe timalemba mʼmakalata tili kutali ndi zomwe tidzakhale tili komweko. |
Pakuti, makalatatu, ati, ndiwo olemera, ndi amphamvu; koma maonekedwe a thupi lake ngofooka, ndi mau ake ngachabe.
Pakuti sitilimba mtima kudziwerenga, kapena kudzilinganiza tokha ndi ena a iwo amene adzivomeretsa okha; koma iwowa, podziyesera okha ndi iwo okha, ndi kudzilinganiza okha ndi iwo okha, alibe nzeru.
Pakuti ndiopa, kuti kaya, pakudza ine, sindidzakupezani inu otere onga ndifuna, ndipo ine ndidzapezedwa ndi inu wotere wonga simufuna; kuti kaya pangakhale chotetana, kaduka, mikwiyo, zilekanitso, maugogodi, ukazitape, zodzikuza, mapokoso;
Chifukwa cha ichi ndilembera izi pokhala palibe ine, kuti pokhala ndili pomwepo ndingachite mowawitsa, monga mwa ulamuliro umene Ambuye anandipatsa ine wakumangirira, ndipo si wakugwetsa.