1 Samueli 9:8 - Buku Lopatulika Ndipo mnyamatayo anayankhanso kwa Saulo nati, Onani m'dzanja langa muli limodzi la magawo anai a sekeli wa siliva; ndidzampatsa munthu wa Mulungu limeneli kuti atiuze njira yathu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mnyamatayo anayankhanso kwa Saulo nati, Onani m'dzanja langa muli limodzi la magawo anai a sekeli wa siliva; ndidzampatsa munthu wa Mulungu limeneli kuti atiuze njira yathu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mnyamatayo adayankha kuti, “Pano ndili ndi kandalama kakang'ono kasiliva, ndipo ndikapereka kwa munthu wa Mulunguyo, kuti atiwuze kumene kwapita abuluwo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mnyamatayo anayankha kuti, “Onani, ndili ndi kandalama kakangʼono ka siliva. Ndikamupatsa munthu wa Mulunguyo ndipo akatidziwitsa kumene kuli abuluwo.” |
Nupite nayo mikate khumi, ndi timitanda, ndi chigulu cha uchi, numuke kwa iye; adzakuuza m'mene umo akhalire mwanayo.
Koma ananena naye, Onatu, m'mzinda muno muli munthu wa Mulungu, ndiye munthu anthu amchitira ulemu; zonse azinena zichitika ndithu; tiyeni tipite komweko, kapena adzakhoza kutidziwitsa zimene tili kuyendera.