Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 14:3 - Buku Lopatulika

3 Nupite nayo mikate khumi, ndi timitanda, ndi chigulu cha uchi, numuke kwa iye; adzakuuza m'mene umo akhalire mwanayo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Nupite nayo mikate khumi, ndi timitanda, ndi chigulu cha uchi, numuke kwa iye; adzakuuza m'mene umo akhalire mwanayo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Utenge mitanda khumi yabuledi, makeke ndiponso botolo la uchi, upite kwa iyeyo. Iye adzakuuza zimene zidzamuwonekere mwanayu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Utenge buledi khumi, makeke ndiponso botolo la uchi ndipo upite kwa mneneriyo. Iye adzakuwuza zimene zidzamuchitikire mwanayu.”

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 14:3
11 Mawu Ofanana  

Mfumu niti kwa munthu wa Mulungu, Tiye kwathu, ukapumule, ndikupatse mphatso.


Ndipo Ahaziya anagwa kuchokera pamwamba pa chipinda chake chosanja chinali ku Samariya, nadwala, natuma mithenga, nanena nayo, Mufunsire kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni ngati ndidzachira nthenda iyi.


Ndipo anadza munthu kuchokera ku Baala-Salisa, nabwera nayo m'thumba mikate ya zipatso zoyamba kwa munthu wa Mulungu, mikate ya barele makumi awiri, ndi ngala zaziwisi za tirigu zosaomba. Ndipo anati, Uwapatse anthu kuti adye.


Pamenepo anabwerera kwa munthu wa Mulungu iye ndi gulu lake lonse, nadzaima pamaso pake, nati, Taonani, tsopano ndidziwa kuti palibe Mulungu padziko lonse lapansi, koma kwa Israele ndiko; ndipo tsopano, mulandire chakukuyamikani nacho kwa mnyamata wanu.


Pamenepo mfumu ya Aramu inati, Tiye, muka, ndidzatumiza kalata kwa mfumu ya Israele. Pamenepo anachoka, atatenga siliva matalente khumi, ndi golide masekeli zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi zovala zakusintha khumi.


anadza kwa Iye mkazi, anali nayo nsupa ya alabastero ndi mafuta onunkhira bwino a mtengo wapatali, nawatsanulira pamutu pake, m'mene Iye analikukhala pachakudya.


Pamenepo alongo ake anatumiza kwa Iye, nanena, Ambuye, onani, amene mumkonda adwala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa