Ndipo mbale wa atate wake wa Saulo ananena kwa iye ndi mnyamata wake, Munanka kuti? Ndipo iye anati, Kukafuna abuluwo; ndipo pakuona kuti sitinawapeze, tinadza kwa Samuele.
1 Samueli 9:10 - Buku Lopatulika Pamenepo Saulo anati kwa mnyamata wake, Wanena bwino; tiye tipite. Chomwecho iwowa anapita kumzinda kumene kunali munthu wa Mulunguyo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Saulo anati kwa mnyamata wake, Wanena bwino; tiye tipite. Chomwecho iwowa anapita kumudzi kumene kunali munthu wa Mulunguyo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Saulo adauza mnyamata wakeyo kuti, “Chabwino. Tiye tizipita.” Choncho adapita kumzinda kumene kunali munthu wa Mulunguko. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Sauli anawuza mnyamata wake kuti, “Chabwino, tiye tipite.” Ndipo ananyamuka kupita ku mzinda umene kunali munthu wa Mulunguyo. |
Ndipo mbale wa atate wake wa Saulo ananena kwa iye ndi mnyamata wake, Munanka kuti? Ndipo iye anati, Kukafuna abuluwo; ndipo pakuona kuti sitinawapeze, tinadza kwa Samuele.
Pakukwera kumzindako anapeza anthu aakazi alikutuluka kuti akatunge madzi, nanena nao, Mlauliyo alipo kodi?
Kale mu Israele, munthu akati afunse kwa Mulungu, ankatero kuti, Tiyeni tipite kwa mlauliyo; popeza iye wotchedwa mneneri makono ano, anatchedwa mlauli kale.