Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 8:9 - Buku Lopatulika

Chifukwa chake tsono umvere mau ao; koma uwachenjeze kolimba, ndi kuwadziwitsa makhalidwe ake a mfumu imene idzawaweruza.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Chifukwa chake tsono umvere mau ao; koma uwachenjeze kolimba, ndi kuwadziwitsa makhalidwe ake a mfumu imene idzawaweruza.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Motero tsono umvere zimene iwowo akunena. Koma ndiye uŵachenjeze kwambiri, ndipo uŵauzitse za mkhalidwe wake wa mfumu imene izidzaŵalamulirayo.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Tsono amvere zimene akunena, koma uwachenjeze kwambiri ndipo uwawuzitse za khalidwe la mfumu imene idzawalamulire.”

Onani mutuwo



1 Samueli 8:9
10 Mawu Ofanana  

Pakuti ndinatsimikizitsa kwa atate anu tsiku lomwe ndinawatulutsa iwo kudziko la Ejipito, mpaka lero lomwe, kuuka mamawa ndi kutsimikiza, kuti, Mverani mau anga.


Ndikanena kwa woipa, Udzafa ndithu, koma iwe osamchenjeza, wosanena kumchenjeza woipayo aleke njira yake yoipa, kumsunga ndi moyo, woipa yemweyo adzafa mu mphulupulu yake; koma mwazi wake ndidzaufuna padzanja lako.


Ndipo kalonga asatengeko cholowa cha anthu kuwazunza, ndi kulanda dziko laolao; apatse ana ake cholowa kulemba dziko lakelake, kuti anthu anga asabalalike, yense kuchoka m'dziko lake.


Pamenepo Samuele anafotokozera anthu machitidwe a ufumu, nawalembera m'buku, nalisunga pamaso pa Yehova. Ndipo Samuele anauza anthu onse amuke, yense kunyumba yake.


Ndipo Samuele anauza Aisraele onse, kuti, Onani ndinamvera mau anu mwa zonse munalankhula ndi ine, ndipo ndinakulongerani mfumu.


Ndipo panali nkhondo yowawa ndi Afilisti masiku onse a Saulo; ndipo Saulo pakuona munthu wamphamvu, kapena ngwazi, anamtenga akhale naye.


Ndipo machitidwe a ansembe akuchitira anthu ndiwo, kuti pamene munthu aliyense akapereka nsembe, mnyamata wa wansembeyo akabwera, nyama ili chiwirire, ndi chovuulira cha ngowe cha mano atatu m'dzanja lake;


Monga ntchito zao zonse anazichita kuyambira tsiku lija ndinawatulutsa ku Ejipito, kufikira lero lino kuti anandisiya Ine, natumikira milungu ina, momwemo alikutero ndi iwenso.