Ndipo zitatha izi, Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa, nalanda Gati ndi midzi yake m'manja a Afilisti.
1 Samueli 7:14 - Buku Lopatulika Ndipo mizinda ya Israele imene Afilisti adailanda kale inabwezedwa kwa Aisraele, kuyambira ku Ekeroni kufikira ku Gati; ndi Aisraele analanditsa midzi yao m'manja a Afilisti. Ndipo pakati pa Aisraele ndi Aamori panali mtendere; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo midzi ya Israele imene Afilisti adailanda kale inabwezedwa kwa Aisraele, kuyambira ku Ekeroni kufikira ku Gati; ndi Aisraele analanditsa milaga yao m'manja a Afilisti. Ndipo pakati pa Aisraele ndi Aamori panali mtendere; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mizinda imene Afilisti anali atalanda idabwezedwanso kwa Aisraele, kuchokera ku Ekeroni mpaka ku Gati. Motero Aisraele adapulumutsa dziko lao kwa Afilisti. Panalinso mtendere pakati pa Aisraele ndi Aamori. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mizinda yonse imene Afilisti analanda kuchokera ku Ekroni mpaka ku Gati inabwezedwa kwa Aisraeli. Choncho Aisraeli anapulumutsa dziko lawo. Ndipo panalinso mtendere pakati pa Aisraeli ndi Aamori. |
Ndipo zitatha izi, Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa, nalanda Gati ndi midzi yake m'manja a Afilisti.
Aamaleke akhala m'dziko la kumwera; ndi Ahiti, ndi Ayebusi, ndi Aamori, akhala ku mapiri, ndi Akanani akhala kunyanja, ndi m'mphepete mwa Yordani.
Ndipo mudzatha mitundu yonse ya anthu amene Yehova Mulungu wanu adzapereka kwa inu; diso lanu lisawachitire chifundo; musamatumikira milungu yao; pakuti uku kudzakuchitirani msampha.
nakawapereka Yehova Mulungu wanu pamaso panu, ndipo mukawakanthe; pamenepo muwaononge konse; musapangana nao pangano, kapena kuwachitira chifundo.
Pamenepo mafumu asanu a Aamori, ndiwo mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yaramuti, mfumu ya ku Lakisi, mfumu ya ku Egiloni anasonkhana, nakwera iwo ndi makamu ao onse namanga misasa pa Gibiyoni, nauthira nkhondo.
natuluka malire kunka ku mbali ya Ekeroni kumpoto; ndipo analemba malire kunka ku Sikeroni, napitirira kuphiri la Baala, natuluka ku Yabinele; ndipo matulukiro a malire anali kunyanja.
Koma Sisera anathawira choyenda pansi ku hema wa Yaele mkazi wa Hebere Mkeni; pakuti panali mtendere pakati pa Yabini mfumu ya Hazori, ndi nyumba ya Hebere Mkeni.