Ndipo m'tsogolo mwake Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa Davide nalanda mudzi wa Metege Ama m'manja mwa Afilisti.
1 Samueli 7:13 - Buku Lopatulika Chomwecho anagonjetsa Afilisti, ndipo iwo sanatumphenso malire a Israele ndipo dzanja la Yehova linasautsa Afilisti masiku onse a Samuele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chomwecho anagonjetsa Afilisti, ndipo iwo sanatumphenso malire a Israele ndipo dzanja la Yehova linasautsa Afilisti masiku onse a Samuele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Afilisti adagonjetsedwa, ndipo sadaloŵenso m'dziko la Aisraele. Chauta ndiye ankalimbana ndi Afilisti nthaŵi yonse Samuele ali moyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero Afilisti anagonjetsedwa ndipo sanadzalowenso mʼdziko la Israeli. Yehova analimbana ndi Afilisti masiku onse a Samueli. |
Ndipo m'tsogolo mwake Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa Davide nalanda mudzi wa Metege Ama m'manja mwa Afilisti.
Ndipo ana a Israele anaonjeza kuchita choipa pamaso pa Yehova; nawapereka Yehova m'dzanja la Afilisti zaka makumi anai.
pakuti taona, udzaima, nudzabala mwana wamwamuna; pamutu pake sipadzafika lumo; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri chibadwire; nadzayamba iye kupulumutsa Israele m'dzanja la Afilisti.
Motero anagonjetsa Amidiyani pamaso pa ana a Israele, osaweramutsanso mitu yao iwowa. Ndipo dziko lidapumula zaka makumi anai m'masiku a Gideoni.
Ndipo Yehova anatumiza Yerubaala, ndi Baraki, ndi Yefita, ndi Samuele, napulumutsa inu m'manja mwa adani anu pozungulira ponse, ndipo munakhala mosatekeseka.
Ndipo kunali atafika nalo, dzanja la Yehova linatsutsa mzindawo ndi kusautsa kwakukulu; ndipo anazunza anthu a mzindawo, aakulu ndi aang'ono; ndi mafundo anawabuka.